Si anthu onse amene amakwaniritsa masomphenya awo ndi ndalama ya ngongole pakuti nthawi zambiri zomwe amaifunila ngongole pa pepala sizimene amagwiritsira ntchito pamene ngongoleyi yawapeza. Isaac Clement Mlombwa omwe amachokera ku Mitundu mfumu yayikulu Chiseka ndiyosiyana ndi mchitidwewu chifukwa iwo ati masomphenya awo tsopano akwaniritsidwa kaamba kangongole ya bungwe la National Economic Empowerment Fund Limited Fund (NEEF) ya Mthirira.
A Mlombwa anali ndi zothina makamaka kuti apeze malo olima, kugula mbeu yabwino yobyala kumunda, feteleza koma kuwapindulira kwa ngongole yokwana MK5,000,000 akwanitsa kugula malo olimapo ma ekala asanu omwe alimapo mbeu zosiyanasiyana. โTizinena zoona ineyo ndidali munthu wovutika koma a NEEF mudandipatsa ngongole ya Ulimi wa Nthirira mudandivuula mโmatope chifukwa ndalamayi yasintha moyo wanga. Pano ndakwanitsa kulima chimanga, tomato, nyemba, anyezi komanso Mabvende,โ Mlombwa kufotokoza.
Iwo ati ngakhale kuti mbeu zambiri sanayambe kukolola koma mbeuzi zachita bwino kwambiri kudimba kwawo ndipo ali ndi chikhulupiriro kuti ulendo wakupha makwacha uja ndi uno.
โChondisangalatsa kwambiri ndi chakuti moyo wanga ukhala odzidalira pa chuma komanso ngongoleyi ikuthandiza anthu omwe amagwira ntchito ku dimba kwanga kuno. Ndakwanitsa kulemba anthu atatu omwe ndikuwalipira mwezi uliwonse kusonyeza kuti pa ntchito 1 miliyoni ine zanga ndapangako zitatu,โ Mlombwa kulongosola.
Dr. Hastings Kamuzu Banda ankapeleka ngongole za ulimi kumakalabu kuti adzichita ulimi ndipo izi zimapangitsa dziko la Malawi kumakhala ndichakudya chochuluka. Pamene anthu ambiri akupitirira kupindula ndi ngongole ya ulimi wa nthirira kuchokera ku bungwe la NEEF, bungweli lalunjika mphamvu zake ku ngongole ya zipangizo za ulimi mโmadera onse mโdziko muno. Alimi ambiri alandira kale feteleza komanso ndalama zomwe zikupelekedwa pansi pa ngongoleyi.