Bungwe la boma lobwereketsa ngongole la National Economic Empowerement Fund (NEEF) lalimbikitsa alimi omwe apindula ndi ngongole ya Ulimi kuti abzyale mitengo mโmadera mwawo ngati njira imodzi yobwezeretsa chilengedwe.
Poyankhula pa mwambo waobzala mitengo mโmudzi mwa Nkhumba, mfumu yayikulu Mwavere mโboma la Mchinji, wamkulu wapampando wa komiti yoyendetsa bungwe la NEEF a Jephta Mtema wati pambali popereka ngongole ya ulimi, bungweli ligwilitsa ntchito anthu omwe akupindula nalo pobwereka ngongoleyi kuti azidzala mitengo.
Iwo anapitirizanso kunena kuti ngongole ya Ulimi yafikira anthu ochuluka ndipo bungweli liri ndi ganizo lakuti chaka chino abzala mitengo yosachepera mazana nkhumi ndi asanu(15,000).
โPamene tapereka matumba osachepera 200,000 a feteleza kwa alimi mazanamazana ifeyo ganizo lathu ndi lakuti alimi amenewa ndi amene atithandize kubzala mitengo imeneyi ndipo bungweli libzala mitengo yosachepera zikwi nkhumi ndi zisanu,ndipo izi tayamba pomwe alimi zikwi zitatu ndi mphambu zisanu ndi omwe alandira mitengo imeneyi kuno kwa Mwavere,โMtema anatero.
Ndipo a Nelson Kumwembe omwe ndi kasitomala wa NEEF amene mwambo wobzala mitengo umachitikira pa munda wawo anati ali ndichimwemwe chachikulu kuti bungwe la NEEF lachita chinthu chomwe sadzayiwala mโmoyo wawo pambali pakuti iye adatenganso ngongole ya ulimi ku bungweli.
โInetu ndikuthokoza kwambiri bungwe la NEEF chifukwa poyamba mudandipatsa ngongole ya ulimi lero mukundipatsanso mitengo. Izitu ndi zosowa kwambiri, tilipo ambiri ku Mchinji kuno koma kufika pondisankha ine ndichinthu chamtengo wapatali.Mundawu ndi ma ekala awiri omwe ponse pabzalidwa mitengo ya mitundu yosiyanasiyana,โ anatero a Kumwembe.
Ena mwa omwe anali nawo ku mwambowu kunali Bwanankubwa wa boma la Mchinji, mayi Lucia Chidalengwa, Phungu wa Nyumba ya Malamulo wa derali, Mayi Agnes Nkusankhoma, wapampando wa ma khansala wa boma la Mchinji, Mayi Dorothy Musa ndi akuluakulu a bungwe la NEEF komanso magulu osiyanasiyana.