NTCHITO YOGAWA FETELEZA WA NGONGOLE YAKHAZIKITSIDWA M’BOMA LA NTCHEU NDI BALAKA
Jan 23, 2025
Boma likuonetsetsa kuti a Malawi akhale ndikuthekela kokolora mbeu zochuluka pomwe alimi ambiri akulandira feteleza wa ngongole kuchokera ku bungwe la NEEF. Inkosi ya Makosi Gomani V yalimbikitsa anthu omwe alandira feteleza wangongoleyu kuti amugwiritse ntchito bwino ndikubweza ngongole pa mwambo okhazikitsa ntchitoyi m’boma la Ntcheu.
“Iyi yomwe mwatenga apa ndi ngongole, ngongole munthu amayenela azibweza, ngongole izi tipindule nazo ndicholinga chakuti tipititse patsogolo ulimi kuno ku Ntcheu” kufotokoza Inkosi Gomani V.
Olemekezeka a Moses Kunkuyu omwe ndi Nduna yofalitsa nkhani, aunikira kuti ngongole ya Zipangizo za Ulimi ipindulire eni ake a Malawi ndikukhala ndi chakudya chokwanira. Iwo anati “Ngongole ya Zipangizo za Ulimi ndi yawina aliyense ndipo yakhazikitsidwa kale m’maboma ambiri, kugawa feteleza wa ngongole kuli mkati ndipo alimi apindula ndi bungwe la NEEF”.
Oimilira komiti yoyendetsa bungwe la NEEF Mai Barbara Banda, ayamikila momwe ntchito yogawa feteleza wa ngongole ikuyendela. Ndipo ndi chikhumbo khumbo cha NEEF kuonetsetsa kuti alimi ambiri apindula ndi ngongole imeneyi.
Alimi oposela 35,000 m’dziko muno ndiwo apindula kale ndi ndondomeko ya Zipangizo za Ulimi ya chaka chino ndipo 35 biliyoni ndiyomwe yagawidwa ngati ndalama komanso feteleza