Anyamata awiri, Richard Banda komanso Charles Peter omwe ndi mamembala a gulu la Kamwendo Traders ochokera m’mudzi mwa Kamwendo Mfumu yayikulu Zulu m’boma la Mchinji amangidwa ndi a Polisi ya Kamwendo powaganizira kuti akugulitsa zipangizo za ulimi zomwe anatenga pangongole ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) Limited.
Anyamatawa ndi mamembala a gulu la Kamwendo Traders ndipo alipo mamembala asanu ndi m’modzi iwowa anafunsa ngongole ya zipangizo za Ulimi ku bungwe la NEEF ndipo adapatsidwa feteleza matumba makumi atatu (30) ngati gulu. Bungwe la NEEF litamva zakugulitsidwa kwa matumbaku silidalekerere koma kuthamangira kumaloko komwe matumba ena alandidwa ndipo anyamatawa atsekeredwa mchitokosi ndipo auzidwa kuti abweze ngongole yomwe adatengayo.
Bungwe la NEEF likupitirira kumemeza anthu onse omwe akutenga ngongole ya mtunduwu makamaka ya zipangizo za ulimi kuti asayerekeze kugulitsa chifukwa kutero ndikusemphana ndi mgwirizano omwe adapanga ndi bungwe la NEEF ndipo wopezeka akugulitsa ayimbidwa mulandu.