• National Economic Empowerment Fund (NEEF), Malawi


post-image
Olemekezeka a Moses Kunkuyu Kalongashawa omwe ndi nduna yazofalitsa nkhani, amema alimi omwe akutenga feteleza wa ngongole yemwe bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) likupeleka mu ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi, kuti adzikumbukila kubweza ngongole yi ndicholinga chofuna kupezetsa ena mwayi ozatenganso ngongoleyi.

Iwo adalankhula izi pa mwambo opeleka fetelezayu m'dera la mfumu a Kuntaja, mu mzinda wa Blantyre komanso kwa Inkosi Bvumbwe ku Thyolo. A Kunkuyu adafotokozanso kuti ali okondwa kuti bungweli likutengapo mbali potumikila ndikuthandiza aMalawi a mzigawo zonse za dziko lino kuthetsa njala, zomwe zingapititsenso patsogolo chitukuko cha mdziko muno.

" Ntchito yanga ngati nthumwi ya boma ndikuonetsetsa kuti feteleza wapelekedwadi kwa alimi oyenela komanso kuchitila umboni kuyi malonjezo ofuna kuthana ndi njala akukwaniritsidwadi kudzela mu ndondomekoyi", kufotokoza a Kunkuyu.

Matumba 300 a feteleza ndiomwe adapelekedwa kwa alimi pa mwambowu ndipo ena 172 adapekeledwa m'dera la Bvumbwe komwe msonkhanowu unapitilila kuchitika.