• National Economic Empowerment Fund (NEEF), Malawi


post-image
Feteleza oposela 112,500 ndiyemwe wagawidwa kale ngati ngongole kwa alimi mโ€™dziko muno pansi pa ngongole ya Zipangizo za Ulimi yomwe imapeleka bungwe la NEEF. Mu ndondomeko ya chaka chino ya Zipangizo za Ulimi bungwe li likupeleka ndalama kapena feteleza.

Mโ€™modzi mwa akulu akulu oyangโ€™anira bungwe la NEEF, a Jacob Mderu, ati ndiosangalala ndi momwe ntchito yi ikuyendela makamaka ku Mchinji komwe anayendela. Mโ€™chaka chino cha ulimi kupereka ngongole ya zipangizo za ulimi ndalama yosachepera 31 Biliyoni kwacha ndiyo yagawidwa kale mdziko muno.

โ€œPofika tsiku la lero tapereka kale ndalama yosachepera 31 biliyoni kwacha pomwe 18.9 biliyoni kwacha yaperekedwa mwa ndalama kuti mulimi iye yekha adzipezere zipangizo za ulimi, ndipo 12.3 biliyoni kwacha ndi yomwe yagawidwa kudzera mu feteleza,โ€ Mderu kufotokoza.

Phungu wa nyumba ya malamulo kuchokera ku chigawo cha kumwera kwa Mchinji, Agness Mkusonkhoma, wayamikira bungwe la NEEF pa ntchito yomwe ikugwira maka yofuna kukwanitsa masomphenya a mtsongoleri wa dziko lino yopititsa patsogolo ulimi.

Boma la Mchinji lapindula nawo ndi matumba oposela 2,093, omwe ndi wokulitsa matumba 1693 komanso wobereketsa 400 ndipo afikira alimi 331 mโ€™madera onse. Ngongole ya Zipangizo za Ulimi ithandiza a Malawi kugonjetsa vuto la njala mโ€™dziko muno.