Olemekeza a Jean Muonawauza Sendeza omwe ndi phungu wa nyumba ya malamulo komanso nduna yowona za kusasiyana pa ntchito pakati pa amayi ndi abambo, alimbikitsa alimi kuti akagwiritse ntchito bwino feteleza wa ngongole omwe bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) likupeleka, posagulitsa kapena kusinthanitsa ndi katundu wina. Iwo adafotokoza izi pa mwambo opeleka fetelezayu omwe unachitika lero pa 7 January,2024 Kwa Mpingu, T/A M'bwatalika m'boma la Lilongwe.
"Ndili okondwela kuti fetelezayu wafikiladi alimi kuno kwa mโbwatalika kutsimikiza kuti ngongoleyi ikuthekadi. Ife ngati nduna za boma tikuyenela kugwirana manja ndi a NEEF komanso mapulogalamu ena angโonoangโono pazochitika ngati izi pofuna kuthetsa njala ndikutukula alimi mdziku munoโ, adatero a Sendeza.
Mwambowu unatsogozedwa ndi nkulu wa bungweli, a Humphrey Mdyetseni omwe akupitilila kuonetsetsa kuti fetelezayu wafikila alimi eni eni ndi kutsindika za kufunikila komugwiritsa ntchito bwino ndi cholinga chofuna kuchepetsa mavuto anjala m'dzikoli.