• National Economic Empowerment Fund (NEEF), Malawi


post-image
Mwambo okhazikitsa kugawa feteleza wa ngongole za zipangizo za ulimi ukupitililabe m'chigawo cha pakati komwe nduna yazofalitsa nkhani, olemekezeka a Moses Kunkuyu akupitiliza kukhazikitsa mwambowu ndi kuonetsetsa kuti alimi alandiladi fetelezayu.

Lero, mwambowu wayamba kuchitika kwa Lobi, m'boma la Dedza komwe kwagawidwa matumba 300 afeteleza kwa magulu asanu ndi atatu ochokela m'bomali ndipo upitilila ku Linthipe ndi Dedza boma.