Pamene chinamtindi cha alimi chikupitirira kusangalala ndi kupatsidwa kwa zipangizo za ulimi kuchokera ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) Limited. Alimi ochokera boma la Mchinji komanso mbali ya kum’mawa kwa Lilongwe ayamikira bungwe la NEEF kaamba kokwaniritsa malonjezano ndi alimiwa maka pa nkhani ya ngongole ya Zipangizo za Ulimi.
Mkulu woyang’anira kayendetsedwe ka kaperekedwe komanso katoleledwe ka ngongole kubungweli, Kisa Kalolokesya ati ndiokondwa ndipo alimi asadandaule chifukwa ulendo uno bungweli lokonzeka kwambiri popereka ngongole ya Zipangizo za Ulimi. NEEF yakonza mgwirizano ndi makamapani omwe amayang’anira za ma inshuwalansi pofuna kuteteza mbeu. Alimi akamafunsa ngongole ku bungweli amapatsidwanso mwayi wotenga inshuwalansi imeneyi kuti iteteze zolima zawo pomwe akumana ndi mavuto ogwa mwadzidzi.
“Lerolino ndine okondwa ngati momwe alimiwa akuvera m’mitima yawo ndipo kupereka zipangizo izi ndi khumbo lathu kuti Malawi komanso anthu akuno ku Mchinji akhale ndi chakudya ndikutukula mabanja awo. Nyengo ndiyosapanganika ndipo sitidawasiye okha alimiwa chifukwa tidapanga mgwiririzano ndi makampani omwe amayang’ana za inshuwalansi ndicholinga chakuti mbeu zikhale zotetezedwa maka ndikusintha kwa nyengoku” Kalolokesya kulankhula.
NEEF ikupitilira kupereka ngongole ya Zipangizo za Ulimi m’maboma onse pomwe alimi akufikilidwa kumadera awo ndi feteleza ndicholinga chochepetsa mavuto ena omwe alimiwa amakumana nawo. Ngongoleyi ithandizira boma kuthetsa njala m’dziko muno komanso kutukula alimi kuti apite patsogolo ndi ulimi wawo.