• National Economic Empowerment Fund (NEEF), Malawi


post-image
Anthu okwana 120 ochokera mmadera a Dedza, Linthipe 1 komanso Nathenje alandira matumba oposa 1200 a feteleza kudzela mu ndondomeko ya ngongole ya zapangizo za Ulimi lero loweruka pa 28 Disembala 2024.
Pa mwambo opeleka fetelezayu, mkulu oyang'anila za chuma ku bungwe la NEEF, Bambo. Benedicto Kananza yemwe amayimilira mkulu wa bungweli, anamemeza onse olandira kuti agwiritse ntchito zipangizozi moyenelela potukula ulimi wawo. Iwo anapempha anthuwa kuti asagulitse fetelezayu.
Mmodzi mwa anthu omwe apindula ndi fetelezayu, a Munila Keniyasi, ochokela ku Linthipe 1, anawonetsa chimwemwe chawo pothokoza bungwe la NEEF popeleka fetelezayu mu nthawi yabwino. Iwo anati fetelezayu awathandizila zedi kuchulukitsa zokolora zawo.