• National Economic Empowerment Fund (NEEF), Malawi


post-image
Gulu la abambo lotchedwa Chilusa lochokela mmudzi wa Kwisinje, mfumu yaikulu Chilunda, boma la Mangochi, lili ndi chimwemwe chodzadza tsaya pomwe alandila matumba a feteleza obeleketsa mbeu okwana 27 kuchokela ku bungwe la NEEF. Iwo adafunsa ngongole ya zipangizo za ulimi ndipo khumbo lawo lakwanilitsidwa tsopano. Abambowa ali ndi chiyembekezo choti akolola zochuluka komanso athana ndi njala yomwe yakhala ikuzunza anthu kwa nthawi yaitali.