Mlimi oyionela patali pano nde wapeza kale feteleza ku bungwe la NEEF lomwe liri kalikiliki kupeleka ngongole ya zipangizo za ulimi m’zigawo zonse za dziko lino. Gulu la abambo lotchedwa Nampeya, lochokela mmudzi wa Ngunga, mfumu yaikulu Chiunda, m’boma la Mangochi lidapempha ngongole ya zipangizo za ulimi ku bungwe la NEEF ndipo apata matumba okwana 25 a feteleza obeleketsa mbeu.