NKONGOKOMWA YOUTH-KUKWANILITSA MASOPHENYA NDI NGONGOLE YA NEEF
Dec 30, 2024
Monga atsogoleri a mawa, achinyamata ayenela kukhala patsogolo ndi ntchito zomwe zingathe kutukula miyoyo yawo. Pofuna kukwanilitsa masomphenya a moyo wawo, gulu la achinyamata la Nkongokomwa lochokela mmudzi wa Wandikanga, mfumu yaikulu Chilunda, m’boma la Mangochi, liri kalikiliki kuchita ntchito za ulimi. Pofuna kutukula ulimiwu, gululi lidapempha ngongole ya zipangizo za ulimi ku bungwe la NEEF ndipo lapata matumba a feteleza obeleketsa mbeu okwana 26.