• National Economic Empowerment Fund (NEEF), Malawi


post-image
Amayi nawo ali patsogolo ndi ntchito za ulimi pofuna kuonetsetsa kuti mawanja awo ali ndi chakudya chokwanila. Mtitimila Women ndi limodzi mwa magulu a amayi omwe achirimika mu ntchito za ulimi. Iwo amachokela mmudzi wa Meso, mfumu yaikulu Chowe, boma la Mangochi ndipo apata matumba a feteleza obeleketsa mbeu okwana 27 kuchokela ku ngongole ya zipangizo za ulimi yomwe adafunsa ku bungwe la NEEF. Mkhala pa mpando wa gululi, a Zione Dickson, ati ndi okondwa ndi thandizoli ndipo ndi othokoza bungwe la NEEF lomwe ndi mlerakhungwa komanso mthandizi wa amayi omwe sakanatha kugula feteleza ochuluka chotele pa iwo okha.