• National Economic Empowerment Fund (NEEF), Malawi


post-image
Mwambo opereka feteleza kwa omwe adatenga ngongole ya zipangizo zaulimi ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) Limited udapitilila m’maboma a Dowa ndi Ntchisi lero pa 30 December 2024.

Pa msonkhanowu, nduna ya zofalitsa nkhani yemwenso ndi mneneri waboma a Moses Kunkuyu adathokoza bungwe la NEEF motsogozedwa ndi wa pampando wa bungweli a Jephta Mtema, Kamba ka ntchito yothandiza alimi powapatsa ngongole ya zipangizo za ulimi, makamaka feteleza yemwe amapelekedwa kwa alimi m’maderawa.

Iwo adathokoza bungweli polingalila mozama popeleka feteleza kwa alimi ngati njira imodzi yothandizira kupitsa patsogolo ulimi. “Ife kwathu ndikulondoloza kuti fetelezayu akupelekedwa kwa anthu oyenera oti akalima dziko lino lithandizika pothetsa vuto la njala komanso kuthandiza kupititsa patsogolo chuma cha dzikoli chomwe chingabwele pogulitsa chimanga ndi mbewu zina ku mayiko akunja”, adatsindika a Kumkuyu.

Bungwe la NEEF motsogozedwa ndi ndunayi apeleka matumba a feteleza okwana 850 kwa alimi 153 m’mabomawa ndipo bungweli lipeleka ngongole zokwana 150 billion Malawi Kwacha mu ndondomekoyi