Pamene nyengo ya mvula ikusendera, alimi osiyanasiyana akusimba lokoma polandila ngongole ya zipangizo za ulimi mu gawo loyamba lopereka ngongole za ulimi ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) Limited.
Mโmodzi mwa alimiwa ndi a Clement Mpoto omwe amachokera mโmudzi mwa Yohane ku Mvera. Iwo ayamikira bungwe la NEEF komanso Boma kamba ka thandizo la ngongole yomwe yabwera munthawi yake. Gulu lomwe ali lotchedwa Chikhasu Mens Club, lapindula nawo ndi ngongole yokwana 12 miliyoni kwacha.
โNgongoleyi ndailandila bwino, ndipo ndili onyadira kwambiri kuti ma pulani anga a ulimi ayenda bwino chaka chino,โ anatero a Mpoto.
Nawo a Memory Chimphanga akusimba lokoma ndi ngongole ya NEEF. Mai olimbikilawa akuchita ulimi wawo kwa Chiwere ku Mvera. Akhala akutenga ngongole ku NEEF kwamaulendo atatu pomwe ulendo uno alandila 3-million-kwacha yomwe yawathandizira kugula zipangizo za ulimi.
โNgongole tailandila nthawi yabwino mvula isanafike, pakadali pano ndizingodikira nthawi yodzala komanso kuthila feteleza,โ anafotokoza mayi Chimphanga.
Alimiwa akwanitsa kugula mbewu, feteleza komanso mankhwala opopera mbewu pokonzekera ulimi wa chaka chino pansi pa ndondomeko ya ngongole ya zipangizo za ulimi ya NEEF.