Ngati njira imodzi yofuna kuwonetsetsa kuti bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) Limited likuyika chidwi pa nkhawa zomwe achinyamata ambiri amakhala nazo, bungweli linachita mikumano ndi achinyamata kuchokera mโmadera osiyanasiyana a mโboma la Lilongwe.
Potsegulira mkumanowu, mkulu wa bungwe la NEEF a Humphrey Mdyetseni, anati ndiokondwa kuti achinyamatawa atadziwa zambiri za ngongole ya NEEF kuti nawo atukule mabizinezi awo. Iwo anati bungwe la NEEF likudzipereka maka polimbikitsa achinyamata kuti akhale odziyimira pawonkha pa chuma.
โNdine osangalala kwambiri chifukwa chakuti achinyamata mukuonetsa chidwi pofuna kutengapo mbali pa nkhani zachuma. Ndikukulimbikitsani pamodzi ndi utsogoleri wanu wa Lilongwe Youth Empowerment Forum kuti mukadziwitsekonso anzanu omwe sanabwere kuno zokhudza ngongole za NEEF,โ Mdyetseni kufotokoza.
Mlembi wa mโchigawo chapakati ku bungwe la Youth Empowerment Forum, a George Nkhoma, ati iwo atawona kuti achinyamata ambiri amawafunsa komwe angapeze thandizo la mpamba wa bizinezi, anaganiza zokafunsa ku bungwe la NEEF kuti liwaphunzitse za mwai wa ngongole omwe ulipo. Mikumano ya ngati iyi ikhala yopindulitsa chifukwa zambiri zomwe zimawapinga kuti atenge ngongole ngati achinyamata tsopano zayankhidwa.
โAnyamata ambiri masiku ano akasowa zochita amangolemba zinthu zopanda pake; mwa ichi ife ngati atsogoleri tinaona kuti kupewa mโchitidwe wotero chinali chazeru kuti tikumane ndi bungwe la NEEF atifotokozere ndondomeko zawo ndikutinso achinyamata ambiri akwanitse kupeza ngongolezi,โ Nkhoma kulongosola.
Bungwe la NEEF limapereka ngongole kwa achinyamata osachepela zaka 18 kufikira 35 zakubadwa. Ngongolezi zimaperekedwa pa gulu ngakhalenso payekha, ndipo chiongola dzanja chake ndi 4.8 pelesenti pa mwezi.