KUTSIMIKIZA KAGWIRITSIDWE NTCHITO KA NGONGOLE YA ZIPANGIZO ZA ULIMI
Nov 26, 2024
Pofuna kuwonetsetsa kuti pulogalamu ya ngongole ya zipangizo za ulimi (farm input loans) ikuyenda bwino, bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) likuchita kafukufuku wotsimikizira momwe alimi omwe atenga ngongoleyi akugwiritsira ntchito. Ndalamazi zikupelekedwa kuti alimi agule feteleza, mbeu, ndi mankhwala othandizira ulimi.
Mkulu wa bungweli, a Humphrey Mdyetseni ndi omwe akutsogolera kafukufukuyi poyendela minda ya alimi am'chigawo cha pakati ndi kumm'wela, kuonetsetsa kuti alimiwa aguladi zipangizo zofunikila ndi ngongoleyi.
"Ngati bungwe la NEEF tili achimwemwe ndi olimbikitsika kuti ngongoleyi ikugwiritsidwa bwino ntchito, pozindikila kuti alimi omwe atenga ngongoleyi akuguladi zipangizo zoyenelela", adatero a Mdyetseni.
Iwo adatsimikizanso za masomphenya ofikila alimi 400 sauzande ndi 150 billion kwacha yomwe apatsidwa ndi boma pofuna kuthandizira kuthana ndi vuto la njala mu m’dziko muno.
A Louis Bvumbwe, a zaka 20 yemwe ndi membala wa gulu la mlimi otsogola la m’mudzi mwa Kwataine m’boma la Ntcheu apindula nawo ndi ndalama yokwana 5 miliyoni kwacha. " Nkutheka ena akuyesa ngati nkhamba kamwa chabe pangongoleyi , ife tili pano kutsimikiza kuti ngongoleyi ikutheka ndipo ikupindula. Ngati gulu takwanitsa kugula matumba 6 aliyense a feteleza, mbewu komanso mankhwala ophela tizilombo ndi 5 miliyoni yomwe tidatenga ngati gulu" a Bvumbwe kufotokoza.
Iwo athokozanso NEEF pokhazikitsa pulogalamuyi yomwe ili ndi phindu komanso tsogolo lothandizira kuthetsa njala mu m'dziko muno.