A Semion Frackson, mlimi yemwe amachokera mโmudzi wa Sosola pansi pa Mfumu yayikulu Chimutu ku Lilongwe, wayamikira bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF), pa ngongole ya ulimi wa mthilira yomwe apindula chaka chino.
Iwo afotokoza kuti ngongoleyi yawathandiza kupeza zinthu zofunika pa ulimi monga zipangizo za ulimi wa mthilira, zomwe zawathandiza kuti akhale ndi chikhulupiliro chokolora phwamwamwa. โNdikuyamikira kwambiri NEEF chifukwa cha thandizo la ngongoleyi. Ndalima chimanga, nyemba komanso tomato ndipo ndikukhulupirira kuti zokololazi zikhala zabwino kwambiri chaka chino. Anzanga ena alima mbatatesi, kabichi ndi ndiwo zamasamba zosiyanasiyana,โ anatero Frackson.
A Frackson ndi m'modzi mwa alimi agulu la Khamalathu Irrigation Scheme, ndipo ati kudzera mu ndondomeko yomwe bungwe la NEEF, ikuchita alimi ochuluka apitilira kutukula miyoyo yawo zomwe zithandizire kusintha momwe chuma chadziko lino chikuyendera.
Pakadali pano bungwe la NEEF, likupitilira kulimbikitsa alimi kuti athamangile kuma ofesi abungweli, ndicholinga choti nawonso athe kupindula ndi ngongole ya zipangizo zakumunda mosavuta.