Kuyambira mwezi wa April 2025, bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF), lakangalika kupeleka ngongole ya zipangizo za ulimi wa mthilira monga feteleza, mbewu ya chimanga, nyemba, mankhwala komanso ma pampu oyendera mphavu ya dzuwa mdziko muno.
Pa 13 komanso 14 August 2025, Mkulu wa bungwe la NEEF, a Humphrey Mdyetseni anayendera magulu alimi kwa mfumu yayikulu Ndindi, Mwanza komanso Makanjira mโboma la Salima. Maguluwa ndi monga Msenza, Funde 1 ndi 2, Chigumukire komanso Makukuta.
Lachisanu pa 15 August 2025, mkuluyi anapitilira kuyendera magulu alimi monga Falawo, Natiyi komanso Kabzyanga ochokera kwa mfumu yayikulu Mwadzama mโboma la Nkhotakota, pomwe ati ndiwonyadira ndizomwe awona. โNdine okondwa komanso kukhutira ndi momwe minda ya alimi ikuchitira kuno ku Salima komanso Nkhotakota ndipo ndili ndi chikhulupiliro kuti alimiwa akolora zochuluka zomwe zichititse kuti mitengo ya chakudya mdziko muno chitsikeโ. Anatero a Mdyetseni.
Mtsogoleri wa gulu la Natiyi Scheme, a Joseph Jelemoti anayamikila bungwe la NEEF kamba kopeleka zipangizozi munthawi yake. โIfe kuno kwathu tikadafa ndi njala popanda NEEF kubwera ku dera lino". Anafotokoza a Jelemoti.
Polankhulapo, Mfumu yayikulu Mwadzama ya mโboma la Nkhotakota inati ndiyokondwa ndi momwe bungwe la NEEF likugwilira ntchito zake polimbikitsa ulimi wa mthilira mโdela lake. โAnthu kuno sadakolore kamba ka ngโamba ndipo popanda NEEF kupeleka ngongole ya zipangizo za ulimi kuno kukadakhala njala yadzaoneniโ. Kufotokoza mfumu yayikulu Mwadzama.
Pakadali pano bungwe la NEEF, lafikira maboma a Salima komanso Nkhotakota ndi ndalama zoposa 5 Billion Kwacha, ku ulimi wa mthilira okha.
#NEEF
#UlimiwaMthilira