Mkulu wa bungwe la National Economic Empowernment Fund (NEEF), a Humphrey Mdyetseni, wati achinyamata akuyenera kudziwa bwino lomwe kufunika kwa bungweli maka pa lingalilo lake lofuna kulimbana ndi njala mdziko muno.
a Mdyetseni anayankhula izi lachinayi m'boma la Ntchisi pa mkumano omwe bungweli linali nawo ndi achinyamata a m'bomali.
Iwo anati achinyamata akuyenera kukhala patsogolo kuthamanga nkumakatenga ngongole zosiyanasiyana monga za ulimi ku bungweli kuti atukule miyoyo yawo. "Achinyamata ambiri mpaka pano simukudziwabe kuti NEEF ili pano chifukwa cha inu, tatiyeni tikatenge ngongole ku bungweli, tithamange ndi ulimi omwe ukhonza kutipindulira". Anatero a Mdyetseni.
M'mawu ake Wapampando wa achinyamata m'bomali a Emmanuel Mdeni, watsimikizira a Mdyetseni kuti tsopano achinyamata apita kubungwelo kukatenga ngongole nsanga kutsatira ndi nkumanowu. "Tikutsimikizileni, ife tibwera ku NEEF kudzatenga ngongole, ndipo tidzabwezanso mu nthawi yoyenera" a Mdeni kufotokoza.
Bungwe la NEEF lili kalikiliki kukumana ndi achinyama m'madera osiyanasiyana kuwadziwitsa komanso kuwalimbikitsa kuti akatenge ngongole ya ulimi wa mthilira komanso ya ulimi wakumunda yomwe ikuyamba m'mwezi wa September.