Kwa zaka zochuluka, aMalawi ambiri akhala akukhamukila ku dziko la South Africa komwe amakapeza ntchito zosiyanasiyana kuti athandizile moyo komanso mabanja awo. Victor Wilfred, wochokela mโmudzi mwa Nyundo, mfumu yaikulu Kuntumanje, mโboma la Zomba naye adali ndi malingaliro opita ku dziko la South Africa kokasaka maganyu koma tsopano ganizoli lasintha kamba koti iye wazilemba yekha ntchito ya ulimi mothandizidwa ndi ngongole ya ulimi wamthilira yomwe bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) Limited likupereka.
Wilfred ndi membala wa gulu la Tiyanjane lomwe lidalandila pump ya madzi yoyendela mphamvu ya dzuwa, matumba 108 a feteleza, (54 NPK, 54 UREA), komanso mbeu ya chimanga kuti ligwiritse ntchito pa munda wa 11 hectares.
Kudzela mu gulu li, Wilfred adalandila matumba awiri a feteleza komanso mbewu ya chimanga yolemela 10kgs kuti agwiritse ntchito pa munda wake wa 1 acre womwe uli ndi chimanga chobiliwila tsopano.
โNdinali ndi malingaliro opita ku Joni koma chifukwa cha kubwela kwa NEEF pano ndilibenso chifukwa chopitila ku Joni. Ndikuthokoza bungwe limeneli chifukwa latiganizila ife achinyamata kuti tisangokhala ayi koma tizigwila ntchito kuti moyo wathu uzipita chitsogolo,โ kufotokoza Wilfred.
Wilfred wati wakhala akuchita ulimi wa chimanga kwa nthawi yaitali koma zokolola zake sizinkafikila matumba khumi kamba kosowa ndalama yogulila zipangizo za ulimi. Pambuyo pa thandizo la NEEF, iye akuyembekezela kukolola chimanga chopitilila matumba 40 ndipo chiyembekezo chake ndi choti nkhani ya njala ikhala mbiri yakale ku banja lake.