Mkulu wa bungwe logawa ngongole la National Economic Empowernment Fund (NEEF) a Humphrey Mdyetseni, walimbikitsa achinyamata a m'maboma a Mwanza ndi Neno ponena kuti ali ndi mwayi waukulu opatsidwa ngongole ndi bungweli kamba koyesetsa kubweza bwino ngongole zawo akatenga ku bungwelo.
A Mdyetseni anayankhula izi ku Mwanza Hotel, pamkumano omwe bungweli linakonza ndi a achinyamata a m'boma la Mwanza ndi Neno pofuna kumva zopsinja zomwe achinyamata akukumana nazo pa nkhani yakatengedwe ndi kabwenzedwe ka ngongole. "Achinyamata am'maboma awiri awa, muli ndi mwayi waukulu oti mukhonza kupindula kwambiri ndi ngongole za NEEF kamba kam'mene mukuchitira kunkhani yobwenza ngongole". Anatero a Mdyetseni.
A Mdyetseni anapitilizanso kuyamikira achinyamatawa powalimbikitsa kuti athamangire ku ofesi za bungweli kuti akatenge ngongole ya ulimi wamthilira yomwe bungweli likupereka pakadali pano.
Pothilirapo ndemanga, wapampando wa achinyamata m'boma la Mwanza a Asani Banda, anayamikira bungwe la NEEF powalora kuchita nawo mkumano ndicholinga chofuna kumva zovuta zawo ndi mgwirizano omwe ulipo pakati pa NEEF ndi achinyamata aku Mwanza komanso Neno ponena kuti Msonkhanowo wawathandizira kudziwa zambiri ndipo achilimika kuti achite bwino ndi ngongole zomwe akutenga ku bungweli. "Tithokoze bungwe lanu la NEEF potilora lero kuti tichite zokambirana. Nsonkhano uno watithandizira kudziwa zambiri ndipo tichilimika ku nkhani ya ulimi". Anatero a Banda.
Pamapeto pake, achinyamata a m'maboma awiriwa atsimikizira bungwe la NEEF kuti athamanga kuma ofesi a bungweri, ndikukatenga ngongole ya ulimi wa mthilira ndicholinga chofuna kukhala nawo mbali yachitukuko cha dziko lino.
Achinyamata a m'boma la Mwanza pakadali pano ali pa 80% pakabwezedwe, ndipo achinyamata a m'boma la Neno ali pa 74%.