MLOOKA PRODUCER COOPERATIVE YALANDIRA NGONGOLE YA MK150 MILIONI YA ULIMI WA MTHILIRA
May 13, 2025
Potsatira kukhazikitsidwa kwa ngongole ya mthilira, Mlooka Producer Cooperative yomwe ili m’dera la TA Mlambe m’boma la Zomba yapatsidwa ngongole ya MK150 miliyoni kuchokera ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF).
Gulu li lili ndima membala 105 omwe 55 ndi amayi ndipo 30 ndi abambo ndipo 20 ndi achinyamata. Ulimi wawo wa mthilira akugwiritsa ntchito madzi ochokera mu m’tsinje wa Shire zomwe zikupeleka chilimibikitso kuti mbewu zawo sizisowa madzi chaka chonse. Malo okwana ma ekala 390 ndi omwe gululi likulima ndipo cholinga cha ngongoleyi ndi kuthandiza alimi a Mlooka kuti apititse patsogolo ulimi wawo, kuchulukitsa zokolola zawo zapa chaka ndikukweza miyoyo yawo.
M’mawu ake, wachiwiri kwa mlembi wa Mlooka producers cooperative, a Chikumbutso Alumpa anati ndi okondwa kwambiri kulandira ngongole ya mthilira yi kuchokela ku NEEF. “ Zipangizo za ulimi zokwanila MK150 miliyoni siza ndalama zochepa, ndipo zitithandiza kwambiri. Tikuthokoza a NEEF chifukwa chakutidalira ife, ndipo ife monga adindo tionetsetsa kuti aliyense wagwiritsa ntchito zipangizo izi moyenelera ndipo tikulonjeza kubweza ngongoleyi mogwirizana ndi malamulo.”
M’modzi mwa nthumwi za NEEF, a Nenani Mponda, analimbikitsa alimiwa kuti agwiritse ntchito zipangizozi mwadongosolo komanso mogwirizana ndi upangili wa alangizi a zaulimi. “Tikuyembekezera kuti ngongole yi isintha m’mene alimi akugwilira ntchito ndipo ithandizira kuthetsa njala kudera kuno pomwe tapeleka mbewu yapamwamba, yocha nsanga ndi feteleza wake,” adatero a Mponda. A Mponda anaonjezera kuti NEEF ikupitiliza kuthandiza magulu a alimi omwe akufuna kusintha miyoyo yawo kudzera mu ngongole yaulimi wa mthilira.
Bungwe la NEEF pakadali pano likupereka zipangizo za ulimi pansi pa ngongole ya Ulimi wa mthilira m’maboma onse m’dziko muno.