NEEF YABZALA MITENGO 1,500 KU MSUKA PRIMARY SCHOOL
Mar 04, 2025
Kupatula ntchito yobweleketsa ngongole zosiyanasiyana kwa nzika za dziko lino, bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) Limited limatengaso mbali pa nkhani yowabwezelako zabwino kwa a Malawi kumbali ya chitukuko pachizungu amati Corporate Social Responsibility. Mitengo yokwana 1, 500 yomwe yabzalidwa pa sukulu ya pulaimale ya Misuka m’boma la Machinga pansi pa udindo obwezela zabwino ku anthu komanso madera.
Mukulankhula kwawo, Mfumu yaikulu Nyambi, yati thandizoli lafika munthawi yake kamba koti sukuluyi ikusowa zinthu zambiri zomwe china mwa icho inali mitengo. Iwo ali ndi chikhulupilira kuti mitengoyi ithandiza kuteteza sukuluyi ku mphepo za nkhuntho zomwe zikumachitika pafupipafupi m’delari. “Ndine okondwa kamba koti chimodzi mwa zosowa za pa sukulu pano chatheka, pali mitengo ya zipatso komanso yopeleka nthuzi kwa ana athu omwe akuphunzila pa sukuluyi” kufotokoza Mfumu yaikulu Nyambi.
Mkulu oyang’anira bungwe la NEEF kuchigawo chakum’mawa, a Victor Mlusu athokoza mafumu, ana a sukulu, makolo komanso aphunzitsi a pasukuluyi kamba kolandira bwino bungwe la NEEF kudelari komanso kukhala ndi chidwi pobwela kudzabzyala mitengoyi. A Mlusu apemphaso anthu kudelari kuti asamale chitukuko chomwe chabwerachi.
Poikilapo ndemanga phungu wadera la Machinga North-East, olemekezeka a Ajiru Kalitendere, wathokoza NEEF kamba ka thandizoli. Iwo anafotokozela kuti linali pempho lawo lomwe linapita ku bungwe la NEEF kuti sukulu ya pulaimale ya Msuka ithandizidwe ndi mitengo pomwe anaona kuti pamapelewela ndipo bungweli linavomeleza pempho lawo. A Kalitendere anenetsa kuti mitengo imeneyi isamalidwa bwino pakuti ndi chitukuto chokhalitsa. “Ndife osangalala kamba koti NEEF yatipatsa mitengo 1,500 ichi ndi chinthu cha mtengo wapatali pakuti sukuluyi ndiyatsopano, ndipo tigwira ntchito limodzi ndi NEEF kuti anthu a dera lino apitilize kutukuka ndi ngongole zosiyana siyana zomwe bungweli likupeleka” kufotokoka a Kalitendere.
Bungwe la NEEF lakwanitsa kale kubyala mitengo yoposela 16,500 ndipo izi zadza pomwe bungweli likulimbikitsa alimi omwe atenga ngongole ya Zipangizo za Ulimi kuti azibyala mitengo pomwe akuchita ulimi. Ndondomeko imeneyi inakhazikitsidwa kale m’boma la Mchinji pa 3 Febuluwale 2025.