• National Economic Empowerment Fund (NEEF), Malawi


post-image
Bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) lalimbikitsa alimi kuti ayikebe chidwi chawo pa ulimi wa mthilira ngati njira imodzi yofuna kupititsa patsogolo kudzidalira kunkhani yachakudya mdziko muno.

Mkulu wa bungwe la NEEF a Humphrey Mdyetseni ndiwo ayankhula izi m’boma la Chikwawa ndi Nsanje komwe amayendera alimi omwe adapindula nawo ndi ngongole ya zipangizo zakumunda yachaka chino.

Polankhula ndi alimi omwe anayendeledwa ku minda yawo a Mdyetseni analimbikitsa alimiwa kuti achilimike ndi ulimi wanthilira maka alimi omwe minda yawo ili m’mbali mwa mitsinje mdera lawo ndicholinga choti apindule ndi ulimi okolola kangapo pachaka “Ndikulimbikitseni alimi kuti chitani gulu la anthu ochuluka lomwe likhonza kutenga ngongole yandalama zochulukanso yomwe imatchedwa cooperative, ndipo ngongole za ulimi wamthirira ziyamba kuperekedwa mu mwezi wa April, amene asankha zipangizo m'malo mwa ndalama adzalandira fetereza ndi mbewu,” anafotokoza motero a Mdyetseni.

M’modzi mwa alimi omwe apindula nawo ndingongoleyi a Mayi Grace Stenala, yemweso ali wapampando wagulu la amayi lotchedwa Chisomo a m’mudzi mwa Nthondo, T/A Tengani, anafotokoza za momwe apindulira ndi ngongoleyi. Iwo anati analandila matumba asanu ndi limodzi a feteleza kudzera ku bungwe la NEEF ndipo anabzala chimanga pa maekala atatu. “Sindinaonepo m’mela wabwino chonchi. Ndinkalima popanda feteleza ndipo ndikakolola kwambiri ndimapeza matumba khumi, asanu ndi atatu 18, koma tsopano, ndikuyembekezera matumba oposa 80 a chimanga kuchokera ku munda womwewo. Zonsezi Kamba kathandizo lomwe ndapeza ku bungwe la NEEF” anatero mokondwera.

Pamwambowu panalinso oimila a mfumu a Nthondo omwe ndi a Madalitso Maxwell, iwo anathokozaso bungwe la NEEF ponena kuti tsopano alimi akutha kubzala mbewu zochuluka zomwe zipangitse kuti chakudya chikhale chikupezeka chaka chonse mdziko muno. “Anthu ambiri m’mudzi muno omwe amakayikira pulogalamuyi tsopano akufuna kulowa nawo. Ndife othokoza ndi ntchito yomwe bungwe la NEEF likuchita osati kwathu kokha kuno komanso m’madera osiyansiyana mdziko muno," a Maxwell anayankhula motero.

Sabata yangothayi, akuluakulu a Bungwe la NEEF akhala akuyendera alimi osiyanasiyana omwe anapindula nawo potenga ngongole ya zipangizo za uli monga feteleza mzigawo zonse za mdiko muno ndicholinga chofuna kudziwa ngati ngongoleyi yathandizadi kutukula miyoyo ya alimi mdziko muno.